Kuunikira sabata yachisanu: Bangwe, Baka ndi Mafco akusakabe chipambano

Matimu a Baka City ,Bangwe All Stars Fc komanso Mafco alephera kupeza chipambano chawo choyamba musabata ya chinayi ya mpikisano wa mpikisano wa TNM.

Musabatayi matimu a Nyasa Big Bullets Fc komanso Fomo ndiwomwe apeza chipambano chawo chachichiwiri pomwe Loweruka lapitali Bullets idagonjetsa 2-1 anyamata a Baka City  ndipo la Mulungu timu ya Fomo Fc inagonjetsa Chitipa United ndi Chigoli chimodzi kwa duu.

Masewero apakati pa Silver ndi Mafco.

Musabatayi munali mapenate okwana atatu Loweruka lapitali Silver Strikers idapezako penate yomwe adagolesa Binwell Katinji pamphindi 34 zamasewero omwe Strikers idachokera kumbuyo kuti igonjetse Mafco 5-1.

Kumbali ina, Kamuzu Barracks idagoletsa kudzera mwa Zeliat Nkhoma pamphindi zokwana 34 zamasewero omwe adagonjesa Civo Service United 2-1 ndipo penate yachitatu mu sabata yachinayi-yi adagoletsa Precious Chiudza wa Mighty Tigers pamphindi zokwana 66 zamasewero omwe Mighty Tigers idagonja 3-1 ndi Karonga United.

Zigoli zokwana 19 ndizomwe zagoletsedwa pa masewero okwana asanu ndi atatu 8 omwe aseweredwa musabata yachinayi yampikisano wu.

Ndipo kufikira pano masewero okwana 32 omwe aseweredwa chiyambireni champikisano-wu pa 6 April 2024 abweretsa zigoli zokwana 78 ndipo zigoli zokwana zisanu zabwera kudzera pa mapenate omwe adapeza matimu a Mighty Mukuru Wanderers,Bangwe All Stars Fc, Kamuzu Barracks,Silver Strikers komanso Mighty Tigers

Padakali pano, katswiri wa timu ya Silver Strikers Adiel  Kaduya ndiyemwe akutsogola kumwetsa zigoli pomwe wagolesa zigoli zokwana zinayi.

Binwel Katinji wa Silver Strikers, Ephram Kondowe wa Nyasa Big Bullets Fc onsewa ali ndi zigoli zokwana zitatu.

Sabata yachisanu ikubweretsa masewero omwe amachedwa kuti Blantyre Derby  omwe alipo loweruka likudzali pa 4 May 2024 ndipo akubwera panthawi imene matimu awiriwa akufanana ma pointi okwana asanu ndi atatu.

Leave A Reply

Your email address will not be published.