M’bindikilo wa Nthanda

Msungwana wotchedwa Nthanda Given Khumbanyiwa yemwe amalimbikitsa ufulu waanthu akuchigwa cha ntsinje wa Shire wakonza m’bindikilo wa yekha ku likulu la nthambi ya Roads Authority munzinda wa Lilongwe.

Nthanda amadziwika bwino pamasamba anchezo pomwe amatulapo nkhawa za anthu am’maboma a Nsanje ndi Chikwawa.

Koma pano wati wapanga chiganizo chowafikira adindo ku offesi zawo kuti akamufotokozere malingalilo awo pa kuonongeka kwa miseu ikulu-ikulu monga Chapananga, Gwanda Chakuamba Highway komanso Sidik Mia Highway.

Iye watinso akufuna Roads Authority, nduna yazachuma, nduna yoona zomanga-manga komanso mtsogoleri wadziko lino afotokoze za milatho ya Miseu Four ndi Ntayamoyo – kapena kuti Chilomo Bridge.

Pakadali pano; amaulendo achepetsa kugwiritsa ntchito mulatho wa Miseu Four omwe umalumikiza maboma awiriwa kamba koti waonongeka ndipo pali chiopsyezo kuti maulendo akhonza kusokonekela mvula ikayamba.

Kumbali inai; anthu akupitilizabe kugwiritsa ntchito mabwato patadutsa zaka zisanu ndi zinai kuchokera pamene Ntayamoyo Bridge inakokoloka.

Pamenepa Nthanda wati achita m’bindikilowu masiku akubwelawa pofuna kudzutsa adindo kuti achitepo kanthu pamalongezano awo okonza miseu Chapananga, Gwanda Chakuamba Highway komanso Sidik Mia Highway komanso milatho ya Miseu Four ndi Ntayamoyo.

“Zikuoneka ngati adindo atiyiwala kuno ku Nsanje ndi Chikwawa ndipo ndikufuna kuwakumbutsa za udindo wawo komanso malongezano awo,” watelo Nthanda.

Leave A Reply

Your email address will not be published.